Jonah 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo amalinyero aja adachita mantha kwambiri, namufunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” Kudziŵa adaadziŵa kuti Yona ankathaŵa Chauta, poti anali ataŵauza kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zinawachititsa mantha kwambiri ndipo anafunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” (Iwo ankadziwa kuti iyeyo amathawa Yehova, chifukwa nʼkuti atawawuza kale).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ici nciani wacicita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.