Jonah 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yonayo adaŵauza kuti, “Chabwino, ingondiponyani m'nyanjamu, mukatero nyanjayi ikhala bata. Ndikudziŵa kuti wolakwa ndine, nkuwona namondweyu akukuvutani chotere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Nyamuleni ndi kundiponya mʼnyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Ndikudziwa kuti wolakwa ndine nʼchifukwa chake chimphepo champhamvuchi chabwera pa inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzacitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkuru amene wakugwerani cifukwa ca ine.