Jonah 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yona pofuna kuthaŵa Chauta, adanyamuka nkumapita ku Tarisisi. Adapita ku mzinda wa Yopa, kumene adapeza chombo chopita ku Tarisisi. Adagula tikiti naloŵa m'chombomo, kuti apite nao ku Tarisisi, kuti choncho athaŵe Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yona anathawa Yehova ndi kulowera ku Tarisisi. Anapita ku Yopa, kumene anapeza sitima yapamadzi yopita ku Tarisisi. Atagula chiphaso, anakwera sitimayo kupita ku Tarisisi kuthawa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako combo comuka ku Tarisi, napereka ndalama zace, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova.