Jonah 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amalinyero adachita mantha, aliyense nkumalirira mulungu wake. Adayamba kuponya katundu m'nyanja kuti chombo chipepuke. M'menemo nkuti Yona atatsikira m'katikati mwa chombo, ali m'tulo tofa nato.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse oyendetsa sitimayo anachita mantha ndipo aliyense anayamba kupemphera kwa mulungu wake. Ndipo anaponya katundu mʼnyanja kuti sitimayo ipepuke. Koma Yona pa nthawiyi nʼkuti atatsikira mʼkatikati mwa sitimayo kumene anagona tulo tofa nato.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato.