Jonah 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adamufunsa kuti, “Tatiwuza, masoka ameneŵa atigwera chifukwa cha yani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nkuti? Ndiwe mtundu wanji?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufumu kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anamufunsa kuti, “Tatiwuze, tsoka limeneli latigwera chifukwa chiyani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nʼkuti? Ndiwe mtundu wanji wa anthu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu coipa ici catigwera cifukwa ca yani? nchito yako njotani? ufuma kuti? dziko lako nliti? nanga mtundu wako?