Jonah 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudandiponya m'nyanja yozama, m'kati mwenimweni mwa njanja, ndipo mweza wam'nyanjamo udandizungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munandiponya mʼnyanja yozama, mʼkati mwenimweni mwa nyanja, ndipo madzi oyenda anandizungulira; mafunde anu onse ndi mkokomo wake zinandimiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, Ndipo madzi anandizinga; Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.