Jonah 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzi adandiyesa m'khosi, nyanja yozama idandizungulira. Udzu wakayandeyande udandikwidzinga m'mutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, madzi akuya anandizungulira, kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Madzi wondimiza anandichititsa mantha, nyanja yozama inandizungulira; udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, Madzi akuya anandizungulira, Kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.