Jonah 2:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidatsikira kunsi ndithu, m'tsinde mwa mapiri, kudziko kumene mipiringidzo idanditsekera mpaka muyaya. Koma Inu Chauta, Mulungu wanga, mudanditulutsa kumandako ndili moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinatsikira ku matsinde a mapiri, Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.