Jonah 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, Ndidzakwaniritsacowindacanga. Cipulumutso nca Yehova.