Jonah 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m'mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osaŵapatsa chilango chimene adaati adzaŵapatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anaona nchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka coipa adanenaci kuti adzawacitira, osacicita.