Jonah 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yona adaloŵa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “Pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Nineve adzapasuka.