Jonah 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m'mapulusa.