Jonah 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analalikira, nanena m'Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analalikira, nanena m'Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;