Jonah 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, nizifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma zipfundidwe ndi ciguduli munthu ndi nyama, nizipfuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yace yoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwace.