Jonah 4:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe udaubzala ndi kuukuza. Udamera pa usiku umodzi, nufanso pa usiku umodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati, Unacitira cifundo msatsiwo umene sunagwirapo nchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;