Jonah 4:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo sindiyenera Ine kodi kucitira cifundo Nineve mudzi waukuru uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?