Jonah 4:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? cifukwa cace ndinafulumira kuthawira ku Tarisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wacisomo ndi wodzala cifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mocuruka, ndi woleka coipaco.