Jonah 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti uchitire Yona mthunzi ndi kumchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, ucite mthunzi pamutu pace, kumlanditsa m'nsautso yace. Ndipo Yona anakondwera kwambiri cifukwa ca msatsiwo.