Jonah 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene dzuŵa linkatuluka, Chauta adautsira Yona mphepo yotentha kuti iwombe kuchokera kuvuma. Dzuŵa lidamtentha pa mutu Yona, mpaka kulenguka nalo. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Nkwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, poturuka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wace wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.