Jonah 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “Inde ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?” Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima cifukwa ca msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.