Joshua 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pitani ku zithando zonse, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu, chifukwa atapita masiku atatu, mudzaoloka Yordani ndi kulandira dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.