Joshua 1:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akazi anu pamodzi ndi ana anu atsalire m'dziko lino la kuvuma kwa Yordani limene Mose adakupatsani. Ng'ombe zanu zitsalenso, koma ankhondo okha pakati panupa ndiwo aoloke atatenga zida, apite kutsogolo kwa Aisraele anzanu kuti akaŵathandize.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordano; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;