Joshua 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo iwowo akadzalandira dzikolo ndi kukhazikikamo, pamenepo ndiye inu mudzabwerere ndi kudzakhala m'dziko lanu limene adakupatsani Mose, mtumiki wa Chauta, konkuno kuvuma kwa Yordani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum'mawa,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanu lanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordano la kum'mawa,