Joshua 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira ku chipululu kumwera, mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kuvuma, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yaikulu kuzambwe, lonseli lidzakhala dziko lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira cipululu, ndi Lebano uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.