Joshua 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kucita monga mwa cilamulo conse anakulamuliraco Mose mtumiki wanga; usacipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukacite mwanzeru kuli konse umukako.