Joshua 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Buku ili la cilamulo lisacoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kucita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzacita mwanzeru.