Joshua 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adonizedeki mfumu ya ku Yerusalemu adamva kuti Yoswa wagonjetsa kotheratu mzinda wa Ai, ndipo waononga mzindawo pamodzi ndi mfumu yake, monga momwe adachitira Yeriko pamodzi ndi mfumu yake yomwe. Adamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni adapangana za mtendere ndi Aisraele, ndipo kuti anali kukhala pakati pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, nizikhala pakati pao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nacitira Ai ndi mfumu yace monga adacitira Yeriko ndi mfumu yace; ndi kuti nzika za Gibeoni zinacitirana mtendere ndi Israyeli, nizikhala pakati pao;