Joshua 10:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankathaŵa nkhondo ya Aisraeleyo kutsika phiri ku Betehoroni mpaka ku Azeka, Chauta adagwetsa miyala yaikulu yamatalala pa iwo kuchokera kumwamba, ndipo idaŵapha. Ophedwa ndi matalala anali ambiri kupambana ophedwa ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.