Joshua 10:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho dzuŵa lidaima pamodzimodzi, ndipo mwezi sudayendenso mpaka Aisraele atagonjetsa adaniwo kotheratu. Zimenezi zidalembedwa m'buku la Yasara. Dzuŵa lidangoima pamodzimodzi pakati pa mutu mu mlengalenga, ndipo silidayendenso mofulumira pafupi tsiku lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho dzuwa linayima, mwezinso unayima, mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake. Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari. Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima Mpaka anthu adabwezera cilango adani ao. Kodi ici sicilembedwa m'buku la Yasari? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.