Joshua 10:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adalamula kuti, “Kunkhuniziranipo miyala pa khomo la phangalo, ndipo muikepo alonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikulu kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yoswa analamula kuti, “Mugubuduzire miyala ikuluikulu pa khomo la phangalo, ndipo muyike anthu ena kuti azilondera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;