Joshua 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inuyo musakhaleko kumeneko. Muŵapirikitse adaniwo, ndipo muŵathire nkhondo kuchokera kumbuyo. Musalole kuti akafike ku mizinda yao. Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani mphamvu zoŵagonjetsera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma inu musaime, pirikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.