Joshua 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu a ku Yerusalemu adachita mantha kwambiri, pakuti Gibiyoni unali mzinda waukulu, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu kupambana Ai, ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mudzi waukulu, monga wina wa midzi yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anaopa kwambiri, popeza Gibeoni ndi mudzi waukuru, monga wina wa midzi yacifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwace, ndi amuna ace onse ndiwo amphamvu.