Joshua 10:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adachita zimenezo: mafumu asanu aja adaŵatulutsadi, mfumu ya ku Yerusalemu, ya ku Hebroni, ya ku Yaramuti, ya ku Lakisi ndi ya ku Egiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatero, natulutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mafumu asanu aja anatulutsidwa, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatero, naturutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.