Joshua 10:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa litangoloŵa, Yoswa adalamula kuti atsitse mafumu aja pamitengopo, ndipo kuti aikidwe m'phanga lomwe ankabisalamolo. Tsono pa khomo la phangalo adatsekapo ndi miyala ikuluikulu, ndipo ikali pomwepo mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzuwa litalowa, Yoswa analamula kuti awachotse pa mitengo ija ndi kuwaponya mʼphanga limene ankabisalamo. Pa khomo pa phangalo anayikapo miyala ikuluikulu imene ilipo mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikuru pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.