Joshua 10:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lomwelo Yoswa adathira nkhondo mzinda wa Makeda naugwira pamodzi ndi mfumu yake. Adapha onse amumzindamo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala wamoyo. Mfumu ya ku Makeda adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lomwelo Yoswa analanda mzinda wa Makeda. Iye anapha anthu a mu mzindamo ndi mfumu yake ndipo sanasiye aliyense wamoyo. Yoswa anachita ndi mfumu ya ku Makeda monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace yom we; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nacitira mfumu ya ku Makeda monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.