Joshua 10:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adapereka mzindawo m'manja mwa Aisraele. Adakantha munthu aliyense mumzindamo ndi lupanga, osasiyapo ndi mmodzi yemwe. Mfumu ya mzindawo adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m'dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Aisraeli. Ndipo Yoswa anapha onse amene anali mu mzindamo. Palibe amene anatsala wamoyo. Ndipo Yoswa anachita ndi mfumu ya Libina monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yace m'dzanja la Israyeli; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namcitira mfumu yace monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.