Joshua 10:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adapatsa Aisraele mphamvu zogonjetsera mzinda wa Lakisi pa tsiku lachiŵiri la nkhondoyo. Tsono monga momwe adachitira ku Libina, sadapulumutsepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israele, ndipo anaulanda tsiku lachiwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anachitira Libina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anapereka Lakisi kwa Israeli; ndipo Yoswa anawulanda pa tsiku lachiwiri. Monga anachita ndi mzinda wa Libina, Yoswa anapha anthu onse okhala mu mzinda wa Lakisi, ndipo palibe amene anatsala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israyeli, ndipo anaulanda tsiku laciwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anacitira Libina.