Joshua 10:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Horamu, mfumu ya ku Gezere, anadza kudzathandiza Lakisi, koma Yoswa adamgonjetsa pamodzi ndi anthu ake omwe, osasiyapo wamoyo ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ake mpaka sanamsiyire ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi nʼkuti Horamu mfumu ya Gezeri itabwera kudzathandiza Lakisi koma Yoswa anamugonjetsa pamodzi ndi asilikali ake ndipo palibe anatsala wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ace mpaka sanamsiyira ndi mmodzi yense.