Joshua 10:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mpaka kuugonjetsa. Adapha ndi lupanga mfumu pamodzi ndi anthu onse amumzindamo, ndi onse a m'midzi yapafupi omwe. Tsono Yoswa adalamula kuti mzindawo auwononge, monga momwe adachitira mzinda wa Egiloni. Palibe ndi mmodzi yemwe m'menemo amene adatsala wamoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anachitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analanda mzindawo napha ndi lupanga mfumu yake pamodzi ndi onse amene ankakhala mʼmenemo. Monga anachita ndi mzinda wa Egiloni, kuti sanasiye aliyense ndi moyo, anachitanso chimodzimodzi ndi mzinda wa Hebroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anacitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.