Joshua 10:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaugonjetsa naulanda pamodzi ndi mfumu yake, kudzanso midzi yoyandikana nawo. Adapha anthu onse akumeneko. Yoswa adauchita mzinda wa Debiri zomwe adauchita mzinda wa Hebroni ndi Libina pamodzi ndi mafumu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naulanda, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiye ndi mmodzi yense; monga anachitira Hebroni momwemo anachitira Debiri ndi mfumu yake, monganso anachitira Libina ndi mfumu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naulanda, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiya ndi mmodzi yense; monga anacitira Hebroni momwemo anacitira Dibiri ndi mfumu yace, monganso anacitira Libina ndi mfumu yace.