Joshua 10:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo. Adagonjetsa mafumu onse m'dziko lamapiri lija, m'dziko lakumwera, m'dziko lakuchigwa ndi lamagomo. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse. Zimenezi ndi zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, adalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero Yoswa anagonjetsa dziko lonselo. Anapha mafumu onse a dera la kumapiri, dera la kummawa, dera la kumadzulo mʼmphepete mwa phiri, ndiponso dera la ku magomo, kummwera. Iye sanasiye wina aliyense wamoyo. Anapha onse amene anali moyo monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli analamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwela, la kucidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyapo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israyeli adalamulira.