Joshua 10:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu asanu a Aamoriwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi ndiponso ya ku Egiloni, adagwirizana. Adasonkhanitsa ankhondo ao nazinga mzinda wa Gibiyoni, ndi kuuthira nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibeoni, nauthira nkhondo.