Joshua 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Gibiyoni adatumiza mau kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja kuti, “Mbuyathu, musatitaye ife atumiki anu. Bwerani msanga mudzatithandize! Tipulumutseni! Mafumu onse a Aamori atsika mapiri kudzamenyana nafe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna a ku Gibeoni anatumira Yoswa mau kucigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.