Joshua 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yoswa adabwera nagonjetsa mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. Nthaŵi imeneyo nkuti mzinda wa Hazori uli wamphamvu kupambana maufumu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yake ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukulu wa maufumu aja onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yace ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukuru wa maufumu aja onse.