Joshua 11:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele adafunkha zinthu zonse zabwino za m'mizinda imeneyo, pamodzi ndi zoŵeta zomwe monga ng'ombe, nazisunga kuti zikhale zao. Koma adani okha adaphedwa onse, osatsala ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israyeli anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.