Joshua 11:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuchokera ku phiri la Halaki kufupi ndi Seiri mpaka ku Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, kumwera kwa phiri la Heremoni. Adapha mafumu ao onse,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuyambira phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri, mpaka Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni patsinde pa phiri la Heremoni; nagwira mafumu ao onse, nawakantha, nawapha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri, mpaka Baala-gadi m'cigwa ca Lebano patsinde pa phiri la Herimoni; nagwira mafwnu ao onse, nawakantha, nawapha.