Joshua 11:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe ndi mfumu imodzi yomwe imene idakambirana zamtendere ndi Aisraele, kupatula Ahivi okha amene ankakhala ku Gibiyoni. Koma ena onse adachita choŵagonjetsa ndi nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe mudzi wakupangana mtendere ndi ana a Israele, koma Ahivi okhala m'Gibiyoni; anaigwira yonse ndi nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe mudzi wakupangana mtendere ndi ana a Israyeli, koma Ahivi okhala m'Gibeoni; anaigwira yonse ndi nkhondo.