Joshua 11:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaŵalimbitsa mtima iwowo kuti alimbane ndi Aisraele, kuti motero aonongeke onse, ndipo aphedwe mopanda chifundo. Zimenezi ndizo zimene Chauta adaalamula Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisrayeli nkhondo kuti iye awaononge konse, kuti asawacitire cifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.