Joshua 11:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyi nkuti Yoswa atapita kukaonongeratu mtundu wa Aanaki. Iwowo anali kukhala m'dziko lija lamapiri, monga ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu ndi ku maiko onse amapiri aja a Yuda ndi a Israele. Yoswa adaŵaononga kwathunthu onsewo ndi mizinda yao yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwachotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israele; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwacotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Dibiri, ku Anabi, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israyeli; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe.