Joshua 11:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe ndi Mwanakimu mmodzi yemwe amene adatsalako m'dziko lonse la Aisraele, komabe ku Gaza, ku Gati ndi ku Asidodi adatsala pang'ono.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma m'Gaza ndi m'Gati ndi m'Asidodi anatsalamo ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israyeli; koma m'Gaza, ndi m'Gati ndi m'Asidodo anatsalamo ena.